1 Ndinapfuulira kwa Yehova mu msauko wanga,Ndipo anandibvomereza,
2 Yehova, landitsani moyo wanga ku milomo ya mabodza,Ndi ku lilime lonyenga.
3 Adzakuninkhanji, adzakuonjezeranji,Lilime lonyenga iwe?
4 Mibvi yakuthwa ya ciphona.Ndi makara tsanya.
5 Tsoka ine, kuti ndiri mlendo m'Meseke,Kuti ndigonera m'mahema a Kedara!
6 Moyo wanga unakhalitsa nthawiPamodzi ndi iye wakudana nao mtendere.
7 Ine ndikuti, Mtendere;Koma polankhula ine, iwowa akuti, Nkhondo.