Masalmo 80 BL92

Apempha Mulungu alanditse anthu ace m'cisautso cao

Kwa Mkulu wa Nyimbo; pa Svosvantmuj locita mboni; Salmo la Asafu.

1 Mbusa wa Israyeli, cherani khutu;Inu wakutsogolera Yosefe ngati nkhosa;Inu wokhala pa akerubi, walitsani.

2 Utsani camuna canu pamaso pa Efraimu ndi Benjamini ndi Manase,Ndipo mutidzere kutipulumutsa.

3 Mutibweze, Mulungu;Nimuwalitse nkhope yanu, ndipo tidzapulumuka.

4 Yehova, Mulungu wa makamu,Mudzakwiyira pemphero la anthu anu kufikira liti?

5 Munawadyetsa mkate wa misozi,Ndipo munawamwetsa misozi yambiri.

6 Mutiika kuti atilimbirane anzathu;Ndipo adani athu atiseka mwa iwo okha,

7 Mulungu wa makamu, mutibweze;Nimuwalitse nkhope yanu, ndipo tidzapulumuka.

8 Mudatenga mpesa kucokera ku Aigupto:Munapitikitsa amitundu ndi kuuoka uwu.

9 Mudasoseratu pookapo,Idagwiritsa mizu yace, ndipo unadzaza dziko.

10 Mthunzi wace unaphimba mapiri,Ndi nthambi zace zikunga mikungudza ya Mulungu.

11 Unatambalitsa mphanda zace mpaka kunyanja,Ndi mitsitsi yace kufikira ku Mtsinje.

12 Munapasuliranii maphambo ace,Kotero kuti onse akupita m'njira acherako?

13 Nguruwe zocokera kuthengo ziukumba,Ndi nyama za kucidikha ziudya,

14 Bwererani, tikupemphani, Mulungu wa makamu;Suzumirani muli m'mwamba, nimupenye, ndi kuzonda mpesa uwu,

15 Ndi tsinde limene dzanja lanu lamanja linaokaeNdi mphanda munadzilimbikitsira.

16 Unapserera ndi moto, unadulidwa;Aonongeka pa kudzudzula kwa nkhope yanu.

17 Dzanja lanu likhale pa munthu wa pa dzanja lamanja lanu;Pa mwana wa munthu amene munadzilimbikitsira.

18 Potero sitidzabwerera m'mbuyo kukusiyani;Titsitsimutseni, ndipo tidzaitanira dzina lanu.

19 Mutibweze, Yehova Mulungu wa makamu;Nimuwalitse nkhope yanu, ndipo tidzapulumuka.