Masalmo 9 BL92

Ayamikira cipulumutso cacikuru

Kwa Mkulu wa Nyimbo; pa Mut-laben. Salmo la Davide.

1 Ndidzayamika Yehova ndi mtima wanga wonse;Ndidzawerengera zodabwiza zanu zonse.

2 Ndidzakondwerera ndi kusekera mwa Inu;Ndidzayimbira dzina lanu, Wam'mwambamwamba Inu.

3 Pobwerera m'mbuyo adani anga,Akhumudwa naonongeka pankhope panu,

4 Pakuti mwandiweruzira mlandu wanga;Mwakhala pa mpando wacifumu, Woweruza wolungama.

5 Mwadzudzula amitundu, mwaononga woipayo,Mwafafaniza dzina lao ku nthawi Yomka muyaya.

6 Adaniwo atha psiti, apululuka nthawi zonse;Ndipo midziyo mwaipasula,Cikumbukilo cao pamodzi catha.

7 Koma Yehova akhala cikhalire:Anakonzeratu mpando wacifumu wace kuti aweruze.

8 Ndipo Iyeyu adzaweruza dziko lapansi m'cilungamo,Nadzaweruza anthu molunjika.

9 Ndipo Yehova adzakhala msanje kwa iye wokhalira mphanthi.Msanje m'nyengo za nsautso;

10 Ndipo iwo akudziwa dzina lanu adzakhulupirira Inu;Pakuti, Inu Yehova, simunawasiya iwo akufuna Inu.

11 Yimbirani zoyamika Yehova, wokhala ku Ziyoni;Lalikirani mwa anthu nchito zace.

12 Pakuti Iye wofuna camwazi awakumbukila;Saiwala kulira kwa ozunzika.

13 Ndicitireni cifundo, Yehova;Penyani kuzunzika kwanga kumene andicitira ondidawo,Inu wondinyamula kundicotsa ku zipata za imfa;

14 Kuti ndibukitse lemekezo lanu lonse;Pa bwalo la mwana wamkazi wa Ziyoni,Ndidzakondwera naco cipulumutso canu.

15 Amitundu anagwa m'mbuna imene anaikumba:Lakodwa phazi lao muukonde anaucha.

16 Anadziwika Yehova, anacita kuweruza:Woipayo anakodwa ndi nchito ya manja ace.

17 Oipawo adzabwerera kumanda,Inde amitundu onse akuiwala Mulungu.

18 Pakuti sadzaiwalika nthawi zonse waumphawi,Kapena ciyembekezo ca ozunzika sicidzaonongeka kosatha.

19 Ukani, Yehova, asalimbike munthu;Amitundu aweruzidwe pankhope panu.

20 Muwacititse mantha, Yehova; Adziwe amitundu kuti ali anthu.