1 Ndinati, Ndidzasunga njira zanga,Kuti ndingacimwe ndi lilime langa:Ndidzasunga pakamwa panga ndi cam'kamwa,Pokhala woipa ali pamaso panga.
2 Ndinatonthola osanena mau, ndinakhala cete osalawa cokoma;Ndipo cisoni canga cinabuka.
3 Mtima wanga unatentha m'kati mwaine;Unayaka moto pakulingirira ine:Pamenepo ndinalankhula ndi lilime langa:
4 Yehova, mundidziwitse cimariziro canga,Ndi mawerengedwe a masiku anga ndi angati;Ndidziwe malekezero anga,
5 Onani, munaika masiku anga akhale monga kuyesa dzanja;Ndipo zaka zanga ziri ngati cabe pamaso panu:Indedi munthu ali yense angakhale wokhazikika, ali cabe konse.
6 Indedi munthu ayenda ngati mthunzi:Indedi abvutika cabe:Asonkhanitsa cuma, ndipo sadziwa adzacilandira ndani?
7 Ndipo tsopano, Ambuye, ndilindira ciani?Ciyembekezo canga ciri pa Inu.
8 Ndipulumutseni kwa zolakwa zangazonse:Musandiike ndikhale cotonza ca wopusa.
9 Ndinakhala du, sindinatsegula pakamwa panga;Cifukwa inu mudacicita.
10 Mundicotsere cobvutitsa canu;Pandithera ine cifukwa ca kulanga kwa dzanja lanu.
11 Pamene mulanga munthu ndi zomdzudzula cifukwa ca mphulupulu,Mukanganula kukongola kwace monga mumacita ndi kadzoce:Indedi, munthu ali yense ali cabe.
12 Imvani pemphero langa, Yehova, ndipo cherani khutu kulira kwanga;Musakhale cete pa misozi yanga:Pakuti ine ndine mlendo ndi Inu,Wosakhazikika, monga makolo anga onse.
13 Ndiloleni, kuti nditsitsimuke,Ndisanamuke ndi kukhala kuli zi.