1 Haleluya.Lemekezani Yehova kocokera kumwamba;Mlemekezeni m'misanje.
2 Mlemekezeni, angelo ace onse;Mlemekezeni, makamu ace onse.
3 Mlemekezeni, dzuwa ndi mwezi;Mlemekezeni, nyenyezi zonse zaunikira.
4 Mlemekezeni, m'mwambamwamba,Ndi madzi inu, a pamwamba pa thambo.
5 Alemekeze dzina la Yehova;Popeza analamulira, ndipo zinalengedwa.
6 Anazikhazikanso ku nthawi za nthawi;Anazipatsa cilamulo cosatumphika.
7 Lemekezani Yehova kocokera ku dziko lapansi,Zinsomba inu, ndi malo ozama onse;
8 Moto ndi matalala, cipale cofewa ndi nkhungu;Mphepo ya namondwe, yakucita mau ace;
9 Mapiri ndi zitunda zonse;Mitengo yazipatso ndi yamikungudza yonse:
10 Nyama za kuthengo ndi zoweta zonse;Zokwawa, ndi mbalame zakuuluka;
11 Mafumu a padziko ndi mitundu yonse ya anthu;Zinduna ndi oweruza onse a padziko;
12 Anyamata ndiponso anamwali;Okalamba pamodzi ndi ana:
13 Alemekeze dzina la Yehova;Pakuti dzina lace lokha ndi lokwezeka;Ulemerero wace uli pamwamba pa dziko lapansi ndi thambo.
14 Ndipo anakweza nyanga ya anthu ace,Cilemekezo ca okondedwa ace onse;Ndiwo ana a Israyeli, anthu a pafupi pa Iye,Haleluya,