1 Ndipfuula nalo liu langa kwa Yehova;Ndi mau anga ndipemba kwa Yehova.
2 Nditsanulirakudandaulakwanga pamaso pace;Ndionetsa msauko wanga pamaso pace.
3 Pamene mzimu wanga unakomoka m'kati mwanga, munadziwa njira yanga.M'njira ndiyendamo anandichera msampha,
4 Penyani ku dzanja lamanja ndipo muone; palibe wondidziwa;Pothawirapo pandisowa; palibe mmodzi wosamalira moyo wanga.
5 Ndinapfuulira kwa inu, Yehova;Ndina, Inu ndinu pothawirapo panga,Gawo langa m'dziko la amoyo.
6 Tamverani kupfuula kwanga; papeza ndisauka kwambiri;Ndilanditseni kwa iwo akundilondola; popeza andilaka.
7 Turutsani moyo wanga m'ndende, kuti ndiyamike dzina lanu;Olungama adzandizinga;Pakuti mudzandicitira zokoma.