Masalmo 18 BL92

Nyimbo yoyamikira Yehova

Kwa Mkulu wa Nyimbo. Salmo la mtumiki wa Yehova, Davide, amene ananena kwa Yehova mau a nyimbo iyi m'mene Yehova anamlanditsa m'dzanja la adani ace onse, ndi m'dzanja la Sauli: ndipo anati,

1 Ndikukondani, Yehova, mphamvu yanga.

2 Yehova ndiye thanthwe langa, ndi linga langa, ndi mpulumutsi wanga;Mulungu wanga, ngaka yanga, ndidzakhulupirira Iye;Cikopa canga, nyanga ya cipulumutso canga, msanje wanga.

3 Ndidzaitanira Yehova, woyenera kutamandika:Ndipo adzandipulumutsa ine kwa adani anga.

4 Zingwe za imfa zinandizinga,Ndipo mitsinje ya zopanda pace inandiopsa.

5 Zingwe za manda zinandizinga:Misampha ya imfa inandifikira ine.

6 M'kusauka kwanga ndinaitana Yehova,Ndipo ndinakuwira Mulungu wanga;Mau anga anawamva m'Kacisi mwace,Ndipo mkuwo wanga wa pankhope pace unalowa m'makutu mwace.

7 Pamenepo linagwedezeka, ndi kutenthemera dziko lapansi.Ndi maziko a mapiri ananjenjemeraNagwedezeka, pakuti anakwiya iyeyo.

8 Unakwera utsi woturuka m'mphuno mwace:Ndi moto wa m'kamwa mwace unanyeka:Nuyakitsa makara.

9 Ndipo Iye anaweramitsa thambo, natsika;Ndipo pansi pa mapazi ace panali mdima bii.

10 Ndipo anaberekeka pa kerubi, nauluka;Nauluka msanga pa mapiko a mphepo,

11 Anaika mdima pobisala pace, hema wace womzinga;Mdima wa madzi, makongwa a kuthambo.

12 Mwa kucezemira kunali pamaso pace makongwa anakanganuka,Matalala ndi makala amoto.

13 Ndipo anagunda m'mwamba Yehova,Ndipo Wam'mwambamwamba anamvetsa liu lace;Matalala ndi makala amoto,

14 Ndipo anatuma mibvi yace nawabalalitsa;Inde mphezi zaunyinji, nawamwaza.

15 Ndipo zidaoneka zoyendamo madzi,Nafukuka maziko a dziko lapansi,Mwa kudzudzula kwanu, Yehova,Mwa mpumo wa mpweya wa m'mphuno mwanu.

16 Anatuma kucokera m'mwamba, ananditenga;Anandibvuula m'madzi ambiri.

17 Anandipulumutsa ine kwa mdani wanga wamphamvu,Ndi kwa iwo ondida ine, pakuti anandiposa mphamvu.

18 Anandipeza ine tsiku la tsoka langa;Koma Yehova anali mcirikizo wanga.

19 Ananditurutsanso andifikitse motakasuka;Anandilanditsa, pakuti anakondwera ndi ine.

20 Yehova anandibwezera monga mwa cilungamo canga;Anandisudzula monga mwa kusisira kwa manja anga.

21 Pakuti ndasunga njira za Yehova,Ndipo sindinacitira coipa kusiyana ndi Mulungu wanga.

22 Pakuti maweruzo ace onse anali pamaso panga,Ndipo malemba ace sindinawacotsa kwa ine.

23 Ndipo ndinakhala wangwiro ndi iye,Ndipo ndinadzisunga wosacita coipa canga.

24 Ndimo anandisudzulira Yehova monga mwa cilungamo canga,Monga mwa kusisira kwa manja anga pamaso pace.

25 Pa wacifundo mukhala wacifundoPa mumthu wangwiro mukhala wangwiro;

26 Pa woyera mtima mukhala woyera mtima;Pa wotsutsatsutsa mukhala wotsutsana naye.

27 Pakuti Inu muwapulumutsa anthu aumphawi;Koma maso okweza muwatsitsa.

28 Pakuti Inu muyatsa nyali yanga;Yehova, Mulungu wanga, aunikira mdima wanga.

29 Pakuti mwa Inu ndipyola khamu la anthu;Ndipo mwa Mulungu wanga ndilumphira linga.

30 Mulungu ndiyewangwiro m'njira zace;Mau a Yehova ngoyengeka; Ndiye cikopa ca onse okhulupirira Iye.

31 Pakuti Mulungu ndani wosati Yehova?Ndipo thanthwe ndani wosati Mulungu wathu?

32 Mulungu ndiye wondizingiza mphamvu m'cuuno,Nakonza njira yanga ikhale yangwiro.

33 Alinganiza mapazi anga ngati a nswala:Nandiimitsa pamsanje panga.

34 Aphunzitsa manja anga agwire nkhondo;Kuti walifuka uta wamkuwa ndi manja anga.

35 Ndipo mwandipatsa cikopa ca cipulumutso canu:Ndipo dzanja lamanja lanu landigwiriziza,Ndipo cifatso canu candikuza ine.

36 Mwandipondetsa patali patali,Sanaterereka mapazi anga.

37 Ndidzalondola adani anga, ndi kuwapeza:Ndipo sindidzabwerera asanathe psiti.

38 Ndidzawapyoza kuti sangakhoze kuuka:Adzagwa pansi pa mapazi anga,

39 Pakuti mwaudizingiza mphamvu m'cuuno ku nkhondoyo:Mwandigonjetsera amene andiukira.

40 Ndipo adani anga mwawalozetsa m'mbuyo kwa ine,Kuti ndipasule ondidawo.

41 Anapfuula, koma panalibewopulumutsa;Ngakhale kwa Yehova, koma sanawabvomereza.

42 Pamenepo ndinawapera ngati pfumbi la kumphepo;Ndinawakhuthula ngati matope a pabwalo.

43 Mwandipulumutsa pa zolimbana nane za anthu;Mwandiika mutu wa amitundu;Mtundu wa anthu sindinaudziwa udzanditumikira.

44 Pakumva m'khutu za ine adzandimvera:Alendo adzandigonjera monyenga.

45 Alendo adzafota,Nadzaturuka monjenjemera m'ngaka mwao.

46 Yehova ngwa moyo; ndipo lidalitsike thanthwe langa;Nakwezeke Mulungu wa cipulumutso canga:

47 Ndiye Mulungu amene andibwe, zerera cilango,Nandigonjetsera mitundu ya anthu.

48 Andipulumutsa kwa adani anga:Inde mundikweza pa iwo akundiukira ine:Mundikwatula kwa munthu waciwawa.

49 Cifukwa cace Yehova ndidzakuyamikani mwa amitundu,Ndipo dzina lanu ndidzaliyimbira.

50 Alanditsa mfumu yace ndi cipulumutso cacikuru:Nacitira cifundo wodzozedwa wace,Davide, ndi mbumba yace, ku nthawi zonse.