1 Imvani pemphero langa, Yehova; ndicherere khutu kupemba kwanga;Ndiyankheni mwa cikhulupiriko canu, mwa cilungamo canu.
2 Ndipo musaitane mlandu wa mtumiki wanu;Pakuti pamaso panu sipadzakhala wolungama wamoyo mmodzi yense.
3 Pakuti mdani alondola moyo wanga;Apondereza pansr moyo wanga;Andikhalitsa mumdima monga iwo adafa kale lomwe.
4 Potero mzimu wanga wakomoka mwa ine;Mtima wanga utenga nkhawa m'kati mwanga,
5 Ndikumbukila masiku a kale lomwe;Zija mudazicita ndilingirirapo;Ndikamba pa ndekha za nchito ya manja anu.
6 Nditambalitsira manja anga kwa Inu:Moyo wanga ulira Inu monga dziko lolira mvula.
7 Fulumirani ndiyankheni, Yehova; mzimu wanga ukutha.Musandibisire nkhope yanu;Ndingafanane nao akutsikira kudzenje.
8 Mundimvetse cifundo canu mamawa;Popeza ndikhulupirira Inu:Mundidziwitse njira ndiyendemo;Popeza ndikweza moyo wanga kwa Inu.
9 Mundilanditse kwa adani anga, Yehova;Ndibisala mwa Inu.
10 Mundiphunzitse cokonda Inu; popeza Inu ndinu Mulungu wanga;Mzimu wanu ndi wokoma; munditsogolere kucidikha.
11 Mundipatse moyo, Yehova, cifukwa ca dzina lanu;Mwa cilungamo canu muturutse moyo wanga m'nsautso.
12 Ndipo mwa cifundo canu mundidulire adani anga,Ndipo muononge onse akusautsa moyo wanga;Pakuti ine ndine mtumiki wanu.