Masalmo 31 BL92

Davide apempha kolimba Mulungu amlanditse, natama cifundo cao, nauzitsa anthu a Mulungu amtame

Kwa Mkulu wa Nyimbo. Salmo la Davide.

1 Ndakhulupirira Inu, Yehova, ndikhale wopanda manyazi nthawi zonse:Mwa cilungamo canu ndipulumutseni ine.

2 Mundicherere khutu lanu; ndipulumutseni msanga:Mundikhalire ine thanthwe lolimba, nyumba yamalinga yakundisunga.

3 Pakuti Inu ndinu thanthwe langa ndi linga langa;Ndipo cifukwa ca dzina lanu ndiyendetseni bwino, ndipo nditsogolereni.

4 Mundionjole m'ukonde umene anandichera mobisika.Pakuti Inu ndinu mphamvu yanga.

5 Ndipereka mzimu wanga m'dzanja lanu:Mwandiombola, Inu Yehova, Mulungu wa coonadi.

6 Ndikwiya nao iwo akusamala zacabe zonama:Koma ndikhulupirira Yehova.

7 Ndidzakondwera ndi kusangalala m'cifundo canu:Pakuti mudapenya zunzo langa;Ndipo mudadziwa mzimu wanga mu nsautso yanga:

8 Ndipo simunandipereka m'dzanja la mdani;Munapondetsa mapazi anga pali malo.

9 Mundicitire cifundo, Yehova, pakuti ndasautsika ine:Diso langa, mzimu wanga, ndi mimba yanga, zapuwala ndi mabvuto,

10 Pakuti moyo wanga watha ndi cisoni, ndi zaka zanga zatha ndi kuusa moyo:Mphamvu yanga yafoka cifukwa ca kusakaza kwanga, ndi mafupa anga apuwala.

11 Ndakhala cotonza cifukwa ca akundisautsa onse,Inde, koposa kwa anansi anga; ndipo anzanga andiyesa coopsa:Iwo akundipenya pabwalo anandithawa.

12 Ndaiwalika m'mtima monga wakufa:Ndikhala monga cotengera cosweka.

13 Pakuti ndamva ugogodi wa ambiri,Mantha andizinga:Pondipangira ciwembu,Anatsimikiza mtima kulanda moyo wanga.

14 Koma ine ndakhulupirira Inu, Yehova:Ndinati, Inu ndinu Mulungu wanga,

15 Nyengo zanga ziri m'manja mwanu:Mundilanditse m'manja a adani anga, ndi kwa iwo akundilondola ine.

16 Walitsani nkhope yanu pa mtumiki wanu:Mundipulumutse ndi cifundo canu.

17 Yehova, musandicititse manyazi; pakuti ndapfuulira kwa Inu:Oipa acite manyazi, atonthole m'manda.

18 Ikhale yosalankhula milomo ya mabodza,Imene imalankhula mwacipongwe pa olungama mtima,Ndi kudzikuza ndi kunyoza.

19 Ha! kukoma kwanu ndiko kwakukuru nanga, kumene munasungira iwo akuopa Inu,Kumene munacitira iwo akukhulupirira Inu, pamaso pa ana a anthu!

20 Pobisalira pamaso panu mudzawabisa kwa ciwembu ca munthu:Mudzawabisa iwo mumsasa kuti muwalanditse pa kutetana kwa malilime.

21 Wolemekezeka Yehova:Pakuti anandicitira cifundo cace codabwiza m'mudzi walinga.

22 Ndipo ine, pakutenga nkhawa, ndinati, Ndadulidwa kundicotsa pamaso panu:Komatu munamva mau a kupemba kwanga pamene ndinapfuulira kwa Inu.

23 Kondani Yehova, Inu nonse okondedwa ace:Yehova asunga okhulupirika,Ndipo abwezera zocuruka iye wakucita zodzitama.

24 Limbikani, ndipo Iye adzalimbitsa mtima wanu,Inu nonse akuyembekeza Yehova.