1 Mudzandiiwala ciiwalire, Yehova, kufikira liti?Mudzandibisira ine nkhope yanu kufikira liti?
2 Ndidzacita uphungu m'moyo mwanga kufikira liti,Pokhala ndi cisoni m'mtima mwanga tsiku lonse?Adzandiukira ine mdani wanga kufikira liti?
3 Penyani, ndiyankheni, Yehova Mulungu wanga:Penyetsani maso anga, kuti ndingagone tulo ta imfa;
4 Kuti anganene mdani wanga, Ndamlaka;Ndipo angakondwere otsutsana nane posunthika ine.
5 Koma ine ndakhulupira pa cifundo canu;Mtima wanga udzakondwera naco cipulumutso canu:
6 Ndidzayimbira Yehova,Pakuti anandicitira zokoma.