Masalmo 33 BL92

Alemekeza Mulungu wolenga, wosunga zonse

1 Pfuulani mokondwera mwa Yehova, inu olungama mtima:Oongoka mtima ayenera kulemekeza.

2 Yamikani Yehova ndi zeze:Myimbireni ndi cisakasa ca zingwe khumi.

3 Mumyimbire Iye Nyimbo yatsopano;Muyimbe mwaluso kumveketsa mau.

4 Pakuti mau a Yehova ali olunjika;Ndi nchito zace zonse zikhulupirika.

5 Iye ndiye wakukonda cilungamo ndi ciweruzo:Dziko lapansi ladzala ndi cifundo ca Yehova.

6 Zakumwamba zinalengedwa ndi mau a Yehova;Ndipo ndi mpweya wa m'kamwa mwace khamu lao lonse.

7 Amaunjika madzi a m'nyanja monga mulu:Amakundika zakudya mosungiramo.

8 Dziko lonse lapansi liope Yehova:Ponse pali anthu acite mantha cifukwa ca Iye,

9 Pakuti ananena, ndipo cinacitidwa;Analamulira, ndipo cinakhazikika.

10 Yehova aphwanya upo wa amitundu:Asandutsa cabe zolingirira za mitundu ya anthu.

11 Ciweruzo ca Yehova cikhazikika cikhazikikire,Zolingirira za m'mtima mwace ku mibadwo mibadwo.

12 Wodalitsika mtundu wa anthu umene Yehova ndiye Mulungu wao;Mtundu womwe anausankha ukhale colandira ca iye yekha.

13 Yehova apenyerera m'mwamba; Aona ana onse a anthu.

14 M'malo akhalamo Iye, amapenya pansiPa onse akukhala m'dziko lapansi;

15 Iye amene akonza mitima ya iwo onse,Amene azindikira zocita zao zonse.

16 Palibe mfumu yoti gulu lalikuru limpulumutsa:Mphamvu yaikuru siicilanditsa ciphona,

17 Kavalo safikana kupulumuka naye:Cinkana mphamvu yace njaikuru sapulumutsa.

18 Taonani, diso la Yehova liri pa iwo akumuopa Iye,Pa iwo akuyembekeza cifundo cace;

19 Kupulumutsa moyo wao kwa imfa,Ndi kuwasunga ndi moyo m'nyengo ya njala.

20 Moyo wathu walindira Yehova:Iye ndiye thandizo lathu ndi cikopa cathu.

21 Pakuti mtima wathu udzakondwera mwa Iye,Cifukwa takhulupirira dzina lace loyera.

22 Yehova, cifundo canu cikhale pa ife,Monga takuyembekezani Inu.