Masalmo 7 BL92

Adani amzinga, Davide adziponya kwa Mulungu

Syigayoni wa Davide woyimbira Yehova, cifukwa ca mau a Kumi Mbenjamini.

1 Yehova Mulungu wanga, ndakhulupirira Inu:Mundipulumutse kwa onse akundilonda, nimundilanditse;

2 Kuti angamwetule moyo wanga ngati mkango,Ndi kuukadzula, wopanda wina wondilanditsa.

3 Yehova Mulungu wanga, ngati ndacita ici;Ngati m'manja anga muli cosalungama;

4 Ngati ndambwezera coipa iye woyanjana ndine;(Inde, ndamlanditsa wondisautsa kopanda cifukwa);

5 Mdani alondole moyo wanga, naupeze;Naupondereze pansi moyo wanga,Naukhalitse ulemu wanga m'pfumbi.

6 Ukani Yehova mu mkwiyo wanu,Nyamukani cifukwa ca ukali wa akundisautsa:Ndipo mugalamukire ine; mwalamulira ciweruzo.

7 Ndipo ukuzingeni msonkhano wa anthu;Ndipo pamwamba pao mubwerere kumka kumwamba.

8 Yehova aweruza anthu mlandu:Mundiweruze, Yehova, monga mwa cilungamo canga, ndi ungwiro wanga uli mwa ine.

9 Ithe mphulupulu ya anthu oipa, ndikupemphani, koma wolungamayo mumkhazikitse:Pakuti woyesa mitima ndi imso ndiye Mulungu wolungama.

10 Cikopa canga ciri ndi Mulungu, Wopulumutsa oongoka mtima.

11 Mulungu ndiye Woweruza walungama,Ndiye Mulungu wakukwiya masiku onse.

12 Akapanda kutembenuka munthu, Iye adzanola lupanga lace;Wakoka uta wace, naupiringidza.

13 Ndipo anamkonzera zida za imfa;Mibvi yace aipanga ikhale yansakali,

14 Taonani, ali m'cikuta ca zopanda pace;Anaima ndi cobvuta, nabala bodza.

15 Anacita dzenje, nalikumba,Nagwa m'mbuna yomwe anaikumba.

16 Cobvuta cace cidzambwerera mwini,Ndi ciwawa cace cidzamgwera pakati pamutu pace.

17 Ndidzayamika Yehova monga mwa cilungamo cace;Ndipo ndidzayimbira Yehova Wam'mwambamwamba.