Masalmo 72 BL92

Za ufumu wa Mfumu yokoma

Salimo la kwa Solomo.

1 Patsani mfumu maweruzo anu, Mulungu,Ndi mwana wa mfumu cilungamo canu.

2 Potero adzanenera anthu anu mlandu ndi m'cilungamo,Ndi ozunzika anu ndi m'ciweruzo.

3 Mapiri adzatengera anthu mtendere,Timapiri tomwe, m'cilungamo.

4 Adzaweruza ozunzika a mwa anthu,Adzapulumutsa ana aumphawi,Nadzaphwanya wosautsa.

5 Adzakuopani momwe likhalira dzuwa ndi mwezi,Kufikira mibadwo mibadwo.

6 Adzanga mvula yakugwa pa udzu wosenga:Monga mvula yothirira dziko.

7 Masiku ace wolungama adzakhazikika;Ndi mtendere wocuruka, kufikira sipadzakhala mwezi.

8 Ndipo adzacita ufumu kucokera kunyanja kufikira kunyanja,Ndi kucokera ku Mtsinje kufikira malekezero a dziko lapansi.

9 Okhala m'cipululu adzagwadira pamaso pace;Ndi adani ace adzaluma nthaka.

10 Mafumu a ku Tarisi ndi ku Zisumbuzo adzabwera naco copereka;Mafumu a ku Sheba ndi Seba adzadza nazo mphatso,

11 Inde mafumu onse adzamgwadira iye:Amitundu onse adzamtumikira.

12 Pakuti adzapulumutsa waumphawi wopfuulayo;Ndi wozunzika amene alibe mthandizi.

13 Adzacitira nsoni wosauka ndi waumphawi,Nadzapulumutsa moyo wa aumphawi,

14 Adzaombola moyo wao ku cinyengo ndi ciwawa;Ndipo mwazi wao udzakhala wa mtengo pamaso pace:

15 Ndipo iye adzakhala ndi moyo; ndipo adzampatsa golidi wa ku Sheba;Nadzampempherera kosalekeza;Adzamlemekeza tsiku lonse.

16 M'dzikomo mudzakhala dzinthu dzocuruka pamwamba pa mapiri;Zipatso zace zidzati waa, ngati za ku Lebano:Ndipo iwo a m'mudzi adzaphuka ngati msipu wapansi.

17 Dzina lace lidzakhala kosatha:Momwe likhalira dzuwa dzina lace lidzamvekera zidzukulu:Ndipo anthu adzadalitsidwa mwa Iye;Amitundu onse adzamucha wodala.

18 Wolemekezeka Yehova Mulungu, Mulungu wa Israyeli,Amene acita zodabwiza yekhayo:

19 Ndipo dzina lace la ulemerero lidalitsike kosatha;Ndipo dziko lonse lapansi lidzale nao ulemerero wace.Amen, ndi Amen.

20 Mapemphero a Davide mwana wa Jese atha.