Masalmo 34 BL92

Davide alemekeza Yehova womlanditsa, nafulumiza ena amtame

Salimo la Davide. Muja anasintha makhalidwe ace pamaso pa Abimeleke, amene anampitikitsa ndipo anacoka.

1 Ndidzalemekeza Yehova nyengo zonse;Kumlemekeza kwace kudzakhala m'kamwa mwanga kosalekeza.

2 Moyo wanga udzatamanda Yehova;Ofatsa adzakumva nadzakondwera.

3 Bukitsani pamodzi ndine ukuru wa Yehova,Ndipo tikweze dzina lace pamodzi.

4 Ndinafuna Yehova ndipo anandibvomera,Nandlianditsa m'mantha anga Onse.

5 Iwo anayang'ana Iye nasanguruka;Ndipo pankhope pao sipadzacita manyazi,

6 Munthu uyu wozunzika anapfuula, ndipo Yehova anamumva,Nampulumutsa m'masautso ace onse.

7 Mngelo wa Yehova azinga kuwacinjiriza iwo akuopa Iye,Nawalanditsa iwo.

8 Talawani, ndipo onani kuti Yehova ndiye wabwino;Wodala munthuyo wakukhulupirira Iye.

9 Opani Yehova, inu oyera mtima ace;Cifukwa iwo akumuopa Iye sasowa.

10 Misona ya mkango isowa nimva njala:Koma iwo akufuna Yehova sadzasowa kanthu kabwino.

11 Idzani ananu ndimvereni ine:Ndidzakulangizani zakumuopa Yehova.

12 Munthu wokhumba moyo ndani,Wokonda masiku, kuti aone zabwino?

13 Uletse lilime lako lisachule zoipa,Ndipo milomo yako isalankhule cinyengo.

14 Pfutuka pazoipa, nucite zabwino,Funa mtendere ndi kuulondola.

15 Maso a Yehova ali pa olungama mtima,Ndipo makutu ace achereza kulira kwao.

16 Nkhopeya Yehovaitsutsananao akucita zoipa,Kudula cikumbukilo cao pa dziko lapansi.

17 Iwowo anaitana, ndipo Yehova anawamva,Nawalanditsa ku masautso ao onse.

18 Yehova ali pafupi ndi iwo a mtimawosweka,Apulumutsa iwo a mzimu wolapadi,

19 Masautso a wolungama mtima acuruka:Koma Yehova amlanditsa mwa onsewa.

20 Iye asunga mafupa ace onse:Silinatyoka limodzi lonse.

21 Mphulupulu idzamupha woipa:Ndipo adzawatsutsa kumlandu iwo akudana naye wolungama.

22 Yehova aombola moyo wa anyamata ace,Ndipo sadzawatsutsa kumlandu onse akukhulupirira Iye.