1 Kwa Inu, Yehova, ndidzapfuulira;Thanthwe langa, musandikhalire ngati wosamva:Pakuti ngati munditontholera ine,Ndidzafanana nao iwo akutsikira kumanda.
2 Mverani mau a kupemba kwanga, pamene ndilirira Inu,Pamene ndikweza manja anga kuloza ponenera panu poyera.
3 Musandikoke kundicotsa pamodzi ndi oipa,Ndi ocita zopanda pace;Amene alankhula zamtendere ndi anansi ao,Koma mumtima mwao muli coipa.
4 Muwapatse monga mwa nchito zao, ndi monga mwa coipa cocita iwo:Muwapatse monga mwa macitidwe a manja ao;Muwabwezere zoyenera iwo.
5 Pakuti sasamala nchito za Yehova,Kapena macitidwe a manja ace,Adzawapasula, osawamanganso.
6 Wodalitsika Yehova,Pakuti adamva mau a kupemba kwanga.
7 Yehova ndiye mphamvu yanga, ndi cikopa canga;Mtima wanga wakhulupirira Iye, ndipo anandithandiza:Cifukwa cace mtima wanga ukondwera kwakukuru;Ndipo ndidzamyamika nayo Nyimbo yanga.
8 Yehova ndiye mphamvu yao,Inde mphamvu ya cipulumutso ca wodzozedwa wace.
9 Pulumutsani anthu anu, ndi kudalitsa colandira canu:Muwawetenso, ndi kuwanyamula nthawi zonse.