Masalmo 51 BL92

Davide abvomereza kucimwa kwace, apempha Mulungu amkhululukire, asamcotsere Mzimu Woyera

Kwa Mkulu wa Nyimbo. Salmo la Davide; m'mene anamdzera Natani mnenertso atalowa iye kwa Bateseba.

1 Mundicitire ine cifundo, Mulungu,Monga mwa kukoma mtima kwanu;Monga mwa unyinji wa nsoni zokoma zanuMufafanize macimo anga.

2 Mubwereze kunditsuka mphulupulu yanga,Ndipo mundiyeretse kundicotsera coipa canga,

3 Cifukwa ndazindikira macimo anga;Ndipo coipa canga ciri pamaso panga cikhalire:

4 Pa Inu, Inu nokha, ndinacimwa,Ndipo ndinacicita coipaco pamaso panu:Kuti mukhale wolungama pakulankhula Inu,Mukhalenso woyera pa kuweruza kwanu.

5 Onani, ndinabadwa m'mphulupulu:Ndipo mai wanga anandilandira m'zoipa.

6 Onani, Inu mukondwera ndi zoonadi m'malo a m'katimo;Ndipo m'malo a m'tseri mudzandidziwitsa nzeru.

7 Mundiyeretse ndi hisope ndipo ndidzayera;Munditsuke ndipo ndidzakhala wa mbu woposa matalala.

8 Mundimvetse cimwemwe ndi kusekera:Kuti mafupawo munawatyola akondwere.

9 Muzibisire nkhope yanu zolakwa zanga,Ndipo mufafanize mphulupulu zanga zonse.

10 Mundilengere mtima woyera, Mulungu;Mukonze mzimu wokhazikika m'kati mwanga.

11 Musanditaye kundicotsa pamaso panu;Musandicotsere Mzimu wanu Woyera.

12 Mundibwezere cimwemwe ca cipulumutso canu;Ndipo mzimu wakulola undigwirizize.

13 Pomwepo ndidzalangiza ocimwa njira zanu;Ndipo olakwa adzabwera kwa Inu.

14 Mundilanditse ku mlandu wa mwazi, Mulungu,Ndinu Mulungu wa cipulumutso canga;Lilime langalidzakweza Nyimbo ya cilungamo canu.

15 Ambuye, tsegulani pa milomo yanga;Ndipo pakamwa panga padzalalikira ulemekezo wanu.

16 Pakuti simukondwera ndi nsembe, mwenzi nditapereka;Nsembe yopsereza simuikonda.

17 Nsembe za Mulungu ndizo mzimu wosweka;Inu, Mulungu, simudzaupeputsa mtima wosweka ndi wolapa.

18 Citirani Ziyoni cokoma monga mwa kukondwera kwanu;Mumange malinga a miyala a Yerusalemu.

19 Pamenepo mudzakondwera nazo nsembe zacilungamo,Ndi nsembe yopsereza ndi yopsereza yathunthu:Pamenepo adzaperekaNg'ombe pa guwa lanu la nsembe.