Masalmo 69 BL92

Davide adandaulira kwa Mulungu cifukwa ca zowawa azimva

Kwa Mkulu wa Nyimbo. Pa Syosyanimu. Salmo la Davide.

1 Ndipulumutseni Mulungu;Pakuti madzi afikira moyo wanga.

2 Ndamira m'thope lozama, lopanda poponderapo;Ndalowa m'madzi ozama, ndipo cigumula candimiza.

3 Ndalema ndi kupfuula kwanga; kum'mero kwauma gwa:M'maso mwanga mwada poyembekeza Mulungu wanga.

4 Ondida kopanda cifukwa acuruka koposa tsitsi la pamutu panga;Ofuna kunditha, ndiwo adani anga monama, ali ndi mphamvu:Pamenepo andibwezetsa cosafunkha ine.

5 Mulungu, mudziwa kupusa kwanga;Ndipo kutsutsika kwanga sikubisikira Inu.

6 Iwo akuyembekeza Inu, Ambuve Yehova wa makamu, asacite manyazi cifukwa ca ine:Iwo ofuna Inu, Mulungu wa Israyeli, asapepulidwe cifukwa ca ine.

7 Pakuti ndalola cotonza cifukwa ca Inu:Cimpepulo cakuta nkhope yanga,

8 Abale anga andiyesa mlendo,Ndi ana a mai wanga andiyesa wa mtundu wina.

9 Pakuti cangu ca pa nyumba yanu candidya;Ndi zotonza za iwo otonza Inu zandigwera ine.

10 Ndipo ndinalira pa kusala kwa moyo wanga,Koma uku kunandikhalira cotonza.

11 Ndipo cobvala canga ndinayesa ciguduli,Koma amandiphera mwambi.

12 Okhala pacipata akamba za ine; Ndipo oledzera andiyimba.

13 Koma ine, pemphero langa liri kwa Inu, Yehova, m'nyengo yolandirika;Mulungu, mwa cifundo canu cacikuru,Mundibvomereze ndi coonadi ca cipulumutso canu.

14 Mundilanditse kuthope, ndisamiremo:Ndilanditseni kwa iwo akundida, ndi kwa madzi ozama.

15 Cigumula cisandifotsere,Ndipo cakuya cisandimize;Ndipo asanditsekere pakamwa pace pa dzenje.

16 Mundiyankhe Yehova; pakuti cifundo canu ncokoma;Munditembenukire monga mwa unyinji wa nsoni zokoma zanu.

17 Ndipo musabisire nkhope yanu mtumiki wanu;Pakuti ndisautsika ine; mundiyankhe msanga.

18 Yandikizani moyo wanga, ndi kuuombola;Ndipulumutseni cifukwa ca adani anga,

19 Mudziwa cotonza canga, ndi manyazi anga, ndi cimpepulo canga:Akundisautsa ali pamaso panu,

20 Cotonza candiswera mtima, ndipo ndidwala ine;Ndipo ndinayembekeza wina wondicitira cifundo, koma palibe;Ndinayembekeza onditonthoza mtima, osawapeza.

21 Ndipo anandipatsa ndulu ikhale cakudya canga;Nandimwetsa vinyo wosasa pomva ludzu ine.

22 Gome lao likhale msampha pamaso pao;Pokhala ndi mtendere iwo, likhale khwekhwe.

23 M'maso mwao mude, kuti asapenye;Ndipo munjenjemeretse m'cuuno mwao kosalekeza.

24 Muwatsanulire mkwiyo wanu, Ndipo moto wa ukali wanu uwagwere.

25 Pokhala pao pakhale bwinja;M'mahema mwao musakhale munthu.

26 Pakuti alondola amene Inu munampanda;Ndipo akambirana za zowawa zao za iwo amene munawalasa.

27 Onjezani mphulupulu pa mphulupulu zao;Ndipo asafikire cilungamo canu.

28 Afafanizidwe m'buku lamoyo,Ndipo asalembedwe pamodzi ndi olungama,

29 Koma ine ndine wozunzika ndi womva zowawa;Cipulumutso canu, Mulungu, cindikweze pamsanje.

30 Ndidzalemekeza dzina la Mulungu ndi kuliyimbira,Ndipo ndidzambukitsa ndi kumyamika.

31 Ndipo cidzakomera Yehova koposa ng'ombe,Inde mphongo za nyanga ndi ziboda,

32 Ofatsa anaciona, nakondwera:Ndipo inu, ofuna Mulungu, mtima wanu ukhale ndi moyo.

33 Pakuti Yehova amvera aumphawi,Ndipo sapeputsa am'ndende ace.

34 Zakumwamba ndi dziko lapansi zimlemekeze,Nyanja ndi zonse zoyenda m'mwemo;

35 Pakuti Mulungu adzapulumutsa Ziyoni, nadzamanga midzi ya Yuda;Ndipo iwo adzakhala komweko, likhale lao lao.

36 Ndipo mbumba ya atumiki ace idzalilandira;Ndipo iwo akukonda dzina lace adzakhalam'mwemo.