Masalmo 55 BL92

Davide adandaula pa kuipa kwa adani, adziponya kwa Mulungu, nalangiza ena azitero iwo omwe

Kwa Mkulu wa Nyimbo: pa Zlrumbu. Cilanliizo ca Davide.

1 Cherani khutu pemphero langa, Mulungu;Ndipo musadzibisa pa kupemba kwanga.

2 Mveram, ndipo mundiyankhe:Ndiliralira m'kudandaula kwanga ndi kubuula;

3 Cifukwa ca mau a mdani,Cifukwa ca kundipsinja woipa;Pakuti andisenza zopanda pace,Ndipo adana nane mumkwiyo.

4 Mtima wanga uwawa m'kati mwanga;Ndipo zoopsa za imfa zandigwera.

5 Mantha ndi kunjenjemera zandidzera,Ndipo zoopsetsa zandikuta.

6 Ndipo ndinati, Ha, wina akadandipatsa mapiko onga a njiwaMwenzi nditauluka, ndi kukhaliratu.

7 Onani, ndikadathawira kutari,Ndikadagona m'cipululu.

8 Ndikadafulumira ndipulumukeKu mphepo yolimba ndi namondwe.

9 Aonongeni, Ambuye, gawani lilime lao:Pakuti ndaona ciwawa ndi ndeu m'mudzimo.

10 Izizo ziuzungulira pa malinga ace usana ndi usiku;Ndipo m'kati mwace muli zapanda pace ndi cobvuta.

11 M'kati mwace muli kusakaza:Ciwawa ndi cinyengo sizicoka m'makwalala ace.

12 Pakuti si mdani amene ananditonzayo;Pakadatero ndikadacilola:Amene anadzikuza pa ine sindiye munthu wondida;Pakadatero ndikadambisalira:

13 Koma ameneyo ndiwe, munthu woyenerana nane,Tsamwali wanga, wodziwana nane.

14 Tinapangirana upo wokoma,Tinaperekeza khamu la anthu popita ku nyumba ya Mulungu.

15 Imfa iwagwere modzidzimutsa,Atsikire kumanda ali amoyo:Pakuti m'mokhala mwao muli zoipa pakati pao,

16 Koma ine ndidzapfuulira kwa Mulungu;Ndipo Yehova atizandipulumutsa.

17 Madzulo, m'mawa, ndi msana ndidzadandaula, ndi kubuula,Ndipo adzamva mau anga.

18 Anaombola moyo wanga ku nkhondo yondilaka, ndikhale mumtendere:Pakuti ndiwo ambiri okangana nane.

19 Mulungu adzamva, nadzawasautsa,Ndiye wokhalabe ciyambire kale lomwe.Popeza iwowa sasinthika konse,Ndipo saopa Mulungu.

20 Anaturutsa manja ace awagwire iwo akuyanjana naye:Anaipsa pangano lace.

21 Pakamwa pace mposalala ngati mafuta amkaka,Koma mumtima mwace munali nkhondo:Mau ace ngofewa ngati mafuta oyenga,Koma anali malupanga osololasolola.

22 Umsenze Yehova nkhawa zako, ndipo Iyeadzakugwiriziza:Nthawi zonse sadzalola wolungama agwedezeke.

23 Koma Inu, Mulungu, mudzawatsitsira ku dzenje la cionongeko:Anthu okhetsa mwazi ndi acinyengo masiku ao sadzafikira nusu;Koma ine ndidzakhulupirira Inu.