1 Mundicitire cifundo, Mulungu, pakuti anthu afuna kundimeza:Andipsinja pondithira nkhondo tsiku lonse.
2 Adani anga afuna kundimeza tsiku lonse:Pakuti ambiri andithira nkhondo modzikuza.
3 Tsiku lakuopa ine,Ndidzakhulupirira Inu.
4 Mwa Mulungu ndidzalemekeza mau ace:Ndakhulupirira Mulungu, sindidzaopa;Anthu adzandicitanji?
5 Tsiku lonse atenderuza mau anga:Zolingirira zao zonse ziri pa ine kundicitira coipa.
6 Amemezana, alalira,Achereza mapazi anga,Popeza alindira moyo wanga.
7 Kodi adzapulumuka ndi zopanda pace?Gwetsani anthu mumkwiyo, Mulungu.
8 Muwerenga kuthawathawa kwanga:Sungani misozi yanga m'nsupa yanu;Kodi siikhala m'buku mwanu?
9 Pamenepo adani anga adzabwerera m'mbuyo tsiku lakuitana ine:Ici ndidziwa, kuti Mulungu abvomerezana nane.
10 Mwa Mulungu ndidzalemekeza mau ace:Mwa Yehova ndidzalemekeza mau ace.
11 Pa Mulungu ndakhulupirira, sindidzaopa;Munthu adzandicitanji?
12 Zowindira Inu Mulungu, ziri pa ine:Ndidzakucitirani zoyamika.
13 Pakuti mwalanditsa moyo wanga kuimfa:Simunatero nao mapazi anga kuti ndingagwe?Kuti ndiyende pamaso pa MulunguM'kuunika kwa amoyo.