Masalmo 68 BL92

Mau akuyamikira Mulungu wa cipulumutso conse

1 Auke Mulungu, abalalike adani ace;Iwonso akumuda athawe pamaso pace.

2 Muwacotse monga utsi ucotseka; Monga phula lisungunuka pamoto,Aonongeke oipa pamaso pa Mulungu.

3 Koma olungama akondwere; atumphe ndi cimwemwe pamaso pa Mulungu;Ndipo asekere naco cikondwerero.

4 Yimbirani Yehova, liyimbireni Nyimbo dzina lace;Undirani mseu Iye woberekekayo kucidikha;Dzina lace ndiye Yehova; ndipo tumphani ndi cimwemwe pamaso pace.

5 Mulungu, mokhala mwace mayera,Ndiye Atate wa ana amasiye, ndi woweruza wa akazi amasiye.

6 Mulungu amangitsira banjaanthu a pa okha;Aturutsa am'ndende alemerere;Koma opikisana naye akhala m'dziko lopanda madzi.

7 Pakuturuka paja, Inu Mulungu, ndi kutsogolera anthu anu,Pakuyenda paja Inu m'cipululu;

8 Dziko lapansi linagwedezeka,Inde thambo linakhapamaso pa Mulungu;Sinai lomwe linagwedezeka pamaso pa Mulungu, Mulungu wa Israyeli.

9 Inu, Mulungu, munabvumbitsa cimvula,Munatsitsimutsa colowa canu pamene cidathodwa.

10 Gulu lanu linakhala m'dziko muja:Mwa ukoma wanu munalikonzera ozunzika, Mulungu.

11 Ambuye anapatsa mau:Akazi akulalikira uthengawo ndiwo khamu lalikuru.

12 Mafumu a magulu a ankhondo athawathawa:Ndipo mkazi amene akhala kwao agawa zofunkha.

13 Pogona inu m'makola a zoweta,Mukhala ngati mapiko a njiwa okulira ndi siliva,Ndi nthenga zace zokulira ndi golidi woyenga wonyezimira.

14 Pamene Wamphamvuyonse anabalalitsa mafumu m'dzikomo,Munayera ngati matalala m'Salimoni.

15 Phiri la Basana ndilo phiri la Mulungu;Phiri la Basana ndilo phiri la mitu mitu.

16 Mucitiranji nsanje mapiri inu a mitu mitu,Ndi phirilo Mulungu analikhumba, akhaleko?Inde, Yehova adzakhalabe komweko kosatha.

17 Magareta a Mulungu ndiwo zikwi makumi awiri, inde zikwi zowirikiza-wirikiza:Ambuye ali pakati pao, monga m'Sinai, m'malo opatulika,

18 Munakwera kumka kumwamba, munapita nao undende kuuyesa ndende;Munalandira zaufulu mwa anthu,Ngakhale mwa opikisana nanu, kuti Yehova Mulungu akakhale nao.

19 Wolemekezeka Ambuye, tsiku ndi tsiku atisenzera katundu,Ndiye Mulungu wa cipulumutso cathu.

20 Mulungu akhala kwa ife Mulungu wa cipulumutso;Ndipo Yehova Ambuye ali nazo zopulumutsira kuimfa.

21 Indedi Mulungu adzaphwanya mutu wa adani ace,Pakati pa mutu pa iye woyendabe m'kutsutsika kwace.

22 Ambuye anati, Ndidzawatenganso ku Basana,Ndidzawatenganso kozama kwa nyanja:

23 Kuti ubviike phazi lako m'mwazi,Kuti malilime a agaru ako alaweko adani ako.

24 Anapenya mayendedwe anu, Mulungu,Mayendedwe a Mulungu wanga, Mfumu yanga, m'malo oyera.

25 Oyimbira anatsogolera, oyimba zoyimba anatsata m'mbuyo,Pakatipo anamwali oyimba mangaka.

26 Lemekezani Mulungu m'masonkhano,Ndiye Ambuye, inu a gwero la Israyeli.

27 Apo pali Benjamini wamng'ono, wakuwacita ufumu,Akuru a Yuda, ndi a upo wao,Akulu a Zebuloni, akulu a Naftali.

28 Mulungu wako analamulira mphamvu yako:Limbitsani, Mulungu, cimene munaticitira.

29 Cifukwa ca Kacisi wanu wa m'YerusalemuMafumu adzabwera naco caufulu kukupatsani.

30 Dzudzulani cirombo ca m'bango,Khamu la mphongo ndi zipfulula za anthu,Yense wakudzigonjera ndi ndarama zasiliva;Anabalalitsa mitundu ya anthu ya kukondwera nayo nkhondo.

31 Akulu adzafumira ku Aigupto;Kushi adzafulumira kutambalitsa manja ace kwa Mulungu.

32 Yimbirani Mulungu, maufumu a dziko lapansi inu;Yimbirani Ambuye zomlemekeza;

33 Kwa Iye wakuberekeka pamwambamwamba, oyambira kale lomwe;Taonani; amveketsa liu lace, ndilo liu lamphamvu.

34 Bvomerezani kuti mphamvu nja Mulungu;Ukulu wace uli pa Israyeli,Ndi mphamvu yace m'mitambo.

35 Inu Mulungu, ndinu woopsa m'malo oyera anu;Mulungu wa Israyeli ndiye amene apatsa anthu ace mphamvu ndi cilimbiko.Alemekezeke Mulungu.