Masalmo 136 BL92

Mulungu alemekezedwe pa cifundo cace

1 Yamikani Yehova pakuti ndiye wabwino:Pakuti cifundo cace ncosatha.

2 Yamikani Mulungu wa milungu:Pakuti cifundo cace ncosatha.

3 Yamikani Mbuye wa ambuye:Pakuti cifundo cace ncosatha.

4 Amene yekha acita zodabwiza zazikuru:Pakuti cifundo cace ncosatha.

5 Amene analenga zakumwamba mwanzeru:Pakuti cifundo cace ncosatha.

6 Amene anayala dziko lapansi pamwamba pa madzi:Pakuti cifundo cace ncosatha.

7 Amene analenga miuni yaikuru:Pakuti cifundo cace ncosatha.

8 Dzuwa liweruze usana:Pakuti cifundo cace ncosatha.

9 Mwezi ndi nyenyezi ziweruze usiku;Pakuti cifundo cace ncosatha.

10 Iye amene anapandira Aaigupto ana ao oyamba:Pakuti cifundo cace ncosatha.

11 Naturutsa Israyeli pakati pao;Pakuti cifundo cace ncosatha.

12 Ndi dzanja lamphamvu, ndi mkono wotambasuka:Pakuti cifundo cace ncosatha.

13 Amene anagawa magawo Nyanja Yofiira:Pakuti cifundo cace ncosatha.

14 Napititsa Israyeli pakati pace;Pakuti cifundo cace ncosatha.

15 Nakhutula Farao ndi khamu lace m'Nyanja Yofiira:Pakuti cifundo cace ncosatha.

16 Amene anatsogolera anthu ace m'cipululu:Pakuti cifundo cace ncosatha.

17 Amene anapanda mafumu akulu:Pakuti cifundo cace ncosatha,

18 Ndipo anawapha mafumu omveka:Pakuti cifundo cace ncosatha.

19 Sihoni mfumu ya Aamori;Pakuti cifundo cace ncosatha.

20 Ndi ogi mfumu ya Basana:Pakuti cifundo cace ncosatha.

21 Ndipo anaperekadzikolaolikhale cosiyira;Pakuti cifundo cace ncosatha.

22 Cosiyira ca kwa Israyeli mtumiki wace;Pakuti cifundo cace ncosatha.

23 Amene anatikumbukila popepuka ife;Pakuti cifundo cace ncosatha.

24 Natikwatula kwa otisautsa;Pakuti cifundo cace ncosatha.

25 Ndiye wakupatsa nyama zonse cakudya;Pakuti cifundo cace ncosatha.

26 Yamikani Mulungu wa kumwamba,Pakuti cifundo cace ncosatha.