Masalmo 103 BL92

Alemekeze Yehovapa cifundo cace cacikuru

Salmo la Da vide.

1 Lemekeza Yehova, moyo wanga;Ndi zonse za m'kati mwanga zilemekeze dzina lace loyera.

2 Lemekeza Yehova, moyo wanga,Ndi kusaiwala zokoma zace zonse aticitirazi:

3 Amene akhululukira mphulupulu zako zonse;Naciritsa nthenda zako zonse;

4 Amene aombola moyo wako ungaonongeke;Nakubveka korona wa cifundo ndi nsoni zokoma:

5 Amene akhutitsa m'kamwa mwako ndi zabwino;Nabweza ubwana wako unge mphungu.

6 Yehova acitira onse osautsidwa Cilungamo ndi ciweruzo.

7 Analangiza Mose njira zace,Ndi ana a Israyeli macitidwe ace.

8 Yehova ndiye wa nsoni zokoma ndi wacisomo,Wosakwiya msanga, ndi wa cifundo cocuruka.

9 Sadzatsutsana nao nthawi zanse;Ndipo sadzasunga mkwiyo wace kosatha.

10 Sanaticitira monga mwa zolakwa zathu,Kapena kutibwezera monga mwa mphulupulu zathu.

11 Pakuti monga m'mwamba mutalikira ndi dziko lapansi,Motero cifundo cace cikulira iwo akumuopa Iye.

12 Monga kum'mawa kutanimpha ndi kumadzulo,Momwemo anatisiyanitsira kutali zolakwa zathu.

13 Monga atate acitira ana ace cifundo,Yehova acitira cifundo iwo akumuopa Iye.

14 Popeza adziwa mapangidwe athu;Akumbukila kuti ife ndife pfumbi.

15 Koma munthu, masiku ace akunga udzu;Aphuka monga duwa la kuthengo.

16 Pakuti mphepo ikapitapo pakhala palibe:Ndi malo ace salidziwanso.

17 Koma cifundo ca Yehova ndico coyambira nthawi yosayamba kufikira nthawi yosatha kwa iwo akumuopa Iye,Ndi cilungamo cace kufikira kwa ana a ana;

18 Kwa iwo akusunga cipangano cace,Ndi kwa iwo akukumbukila malangizo ace kuwacita.

19 Yehova anakhazika mpando wacifumu wace Kumwamba;Ndi ufumu wace ucita mphamvu ponsepo,

20 Lemekezani Yehova, inu angelo ace;A mphamvu zolimba, akucita mau ace,Akumvera liu la mau ace.

21 Lemekezani Yehova, inu makamu ace onse;Inu atumiki ace akucita comkondweretsa Iye,

22 Lemekezani Yehova, inu, nchito zace zonse,Ponse ponse pali ufumu wace:Lemekeza Yehova, moyo wanga iwe.