1 Akapanda kumanga nyumba Yehova,Akuimanga agwiritsa nchito cabe;Akapanda kusunga mudzi Yehoya,Mlonda adikira cabe.
2 Kuli cabe kwa inu Rulawirira mamawa ndi kusagonerapo madzulo,Kudya mkate wosautsa kuupeza;Kuli tero kuti izi apatsa okondedwa ace ngati m'tulo.
3 Taonani ana ndiwo colandira ca kwa Yehova;Cipatso ca m'mimba ndico mphotho yace.
4 Ana a ubwana wace wa munthuAkunga mibvi m'dzanja lace la ciphona.
5 Wodala munthu amene anadzaza nayo phodo lace:Sadzacita manyazi iwo,Pakulankhula nao adani kucipata.