Masalmo 102 BL92

Wopsinjika apempha Mulungu acitire anthu ace cifundo, amitundu nammverenso

Pemphero la Wozunzika, m'mene anakomoka natsanulira cobnaatira cace pamaso pa Yehova,

1 Yehova, imvani pemphero langa,Ndipo mpfuu wanga ufikire Inu.

2 Musandibisire nkhope yanu tsiku la nsautso yanga;Mundichereze khutu lanu;Tsiku limene ndiitana ine mundiyankhe msanga,

3 Popeza masiku anga akanganuka ngati utsi,Ndi mafupa anga anyeka ngati nkhuni.

4 Mtima wanga ukunga udzu wamweta, nufota;Popeza ndiiwala kudya mkate wanga.

5 Cifukwa ca liu la kubuula kwangaMnofu wanga umamatika ku mafupa anga.

6 Ndikunga bvuwo m'cipululu;Ndikhala ngati kadzidzi wa kumabwinja.

7 Ndidikira, ndikhala ngati mbawaIri yokha pamwamba pa tsindwi.

8 Adani anga anditonza tsiku lonse;Akundiyarukirawo alumbirira ine.

9 Pakuti ndadya mapulusa ngati mkate,Ndi kusanganiza-comwera canga ndi misozi,

10 Cifukwa ca ukali wanu ndi kuzaza kwanu;Popeza munandinyamula ndipo munandigwetsa.

11 Masiku anga akunga mthunzi womka m'tali;Ndipo ine ndauma ngati udzu.

12 Koma Inu, Yehova, mukhalabe ku nthawi yonse;Ndi cikumbukilo canu ku mibadwo mibadwo.

13 Inu mudzauka, ndi kucitira nsoni Ziyoni;Popeza yafika nyengo yakumcitira cifundo, nyengo yoikika.

14 Pakuti atumiki anu akondwera nayo miyala yace,Nacitira cifundo pfumbi lace.

15 Pamenepo amitundu adzaopa dzina la Yehova,Ndi mafumu onse a dziko lapansi ulemerero wanu;

16 Pakuti Yehova anamanga Ziyoni,Anaoneka m'ulemerero wace;

17 Anasamalira pemphero la iwo akusowa konse,Osapepula pemphero lao.

18 Ici adzacilembera mbadwo ukudza;Ndi mtundu wa anthu umene udalengedwa udzamlemekeza Yehova.

19 Pakuti anapenya pansi ali kumwamba kuli malo ace opatulika;Yehova pokhala kumwamba anapenya dziko lapansi;

20 Kuti amve kubuula kwa wandende;Namasule ana a imfa,

21 Kuti anthu alalikire dzina la Yehova m'Ziyoni,Ndi cilemekezo cace m'Yerusalemu;

22 Posonkhana pamodzi mitundu ya anthu,Ndi maufumu kuti atumikire Yehova.

23 Iye analanda mphamvu yanga panjira;Anacepsa masiku anga.

24 Ndinati, Mulungu wanga, musandicotse pakati pa masiku anga:Zaka zanu zikhalira m'mibadwo mibadwo.

25 Munakhazika dziko lapansi kalelo;Ndipo zakumwamba ndizo nchito ya manja anu.

26 Zidzatha izi, koma Inu mukhala:Inde, zidzatha zonse ngati cabvala;Mudzazisintha ngati maraya, ndipo zidzasinthika:

27 Koma Inu ndinu yemweyo,Ndi zaka zanu sizifikira kutha.

28 Ana a atumiki anu adzakhalitsa,Ndi mbeu zao zidzakhazikika pamaso panu.