Masalmo 49 BL92

Za pansi pano nza cabe

Kwa Mkulu wa Nyimbo; Salmo la ana a Kora.

1 Dzamveni kuno, anthu inu nonse;Cherani khutu, inu nonse amakono,

2 Awamba ndi omveka omwe,Acuma ndi aumphawi omwe.

3 Pakamwa panga padzanena zanzeru;Ndipo cilingiriro ca mtima wanga cidzakhala ca cidziwitso.

4 Ndidzachera khutu kufanizo:Ndidzafotokozera cophiphiritsa canga poyimbira.

5 Ndidzaoperanji masiku oipa,Pondizinga amphulupulu onditsata kucidendene?

6 Iwo akutama kulemera kwao;Nadzitamandira pa kucuruka kwa cuma cao;

7 Kuombola mbale sangadzamuombole,Kapena kumperekera dipo kwa Mulungu:

8 (Popeza ciombolo ca moyo wao nca mtengo wace wapatali,Ndipo cilekeke nthawi zonse)

9 Kuti akhale ndi moyo osafa,Osaona cibvundi.

10 Pakuti aona anzeru amafa,Monga aonongekera wopusa, wodyerera momwemo,Nasiyira ena cuma cao.

11 Mumtima mwao ayesa kuti nyumba zao zikhala cikhalire,Ndi mokhala iwo ku mibadwo mibadwo;Achapo dzina lao padziko pao.

12 Koma munthu wa ulemu wace sakhalitsa:Afanana ndi nyama za kuthengo, afanana nazo.

13 Njira yao yino ndiyo kupusa kwao:Koma akudza m'mbuyo abvomereza mau ao.

14 Aikidwa m'manda ngati nkhosa;Mbusa wao ndi imfa:Ndipo m'mawa mwace oongoka mtima adzakhala mafumu ao;Ndipo maonekedwe ao adzanyekera kumanda, kuti pokhala pace padzasowa.

15 Koma Mulungu adzaombola moyo wanga ku mphamvu ya manda:Pakuti adzandilandira ine.

16 Usaope polemezedwa munthu,Pocuruka ulemu wa nyumba yace;

17 Pakuti pomwalira iye sadzamuka nako kanthu kali konse;Ulemu wace sutsika naye kumtsata m'mbuyo.

18 Angakhale anadalitsa moyo wace pokhala ndi moyo,Ndipo anthu akulemekeza iwe, podzicitira wekha zokoma,

19 Adzamuka ku mbadwo wa makolo ace;Sadzaona kuunika nthawi zonse.

20 Munthu waulemu, koma wosadziwitsa,Afanana ndi nyama za kuthengo, afanana nazo.