1 Lemekeza Yehova, moyo wanga;Ndi zonse za m'kati mwanga zilemekeze dzina lace loyera.
2 Lemekeza Yehova, moyo wanga,Ndi kusaiwala zokoma zace zonse aticitirazi:
3 Amene akhululukira mphulupulu zako zonse;Naciritsa nthenda zako zonse;
4 Amene aombola moyo wako ungaonongeke;Nakubveka korona wa cifundo ndi nsoni zokoma:
5 Amene akhutitsa m'kamwa mwako ndi zabwino;Nabweza ubwana wako unge mphungu.