9 Sadzatsutsana nao nthawi zanse;Ndipo sadzasunga mkwiyo wace kosatha.
10 Sanaticitira monga mwa zolakwa zathu,Kapena kutibwezera monga mwa mphulupulu zathu.
11 Pakuti monga m'mwamba mutalikira ndi dziko lapansi,Motero cifundo cace cikulira iwo akumuopa Iye.
12 Monga kum'mawa kutanimpha ndi kumadzulo,Momwemo anatisiyanitsira kutali zolakwa zathu.
13 Monga atate acitira ana ace cifundo,Yehova acitira cifundo iwo akumuopa Iye.
14 Popeza adziwa mapangidwe athu;Akumbukila kuti ife ndife pfumbi.
15 Koma munthu, masiku ace akunga udzu;Aphuka monga duwa la kuthengo.