1 Yamikani Yehova pakuti Iye ndiye wabwino;Pakuti cifundo cace ncosatha.
2 Atere oomboledwa a Yehova,Amene anawaombola m'dzanja la wosautsa;
3 Nawasokolotsa kumaiko,Kucokera kum'mawa ndi kumadzulo,Kumpoto ndi kunyanja.
4 Anasokera m'cipululu, m'njira yopanda anthu;Osapeza mudzi wokhalamo.
5 Anamva njala ndi ludzu,Moyo wao unakomoka m'kati mwao.
6 Pamenepo anapfuulira kwa Yehova mumsauko mwao,Ndipo anawalanditsa m'kupsinjika kwao.