14 Anawaturutsa mumdima ndi mu mthunzi wa imfa,Nadula zomangira zao.
15 Ayamike Yehova cifukwa ca cifundo cace,Ndi zodabwiza zace za kwa ana a anthu!
16 Popeza adaswa zitseko zamkuwa,Natyola mipiringidzo yacitsulo.
17 Anthu opusa azunzika cifukwa ca zolakwa zao,Ndi cifukwa ca mphulupulu zao.
18 Mtima wao unyansidwa naco cakudya ciri conse;Ndipo ayandikira zipata za imfa.
19 Pamenepo apfuulira kwa Yehova m'kusauka kwao,Ndipo awapulumutsa m'kupsinjika kwao.
20 Atumiza mau ace nawaciritsa,Nawapulumutsa ku cionongeko cao.