16 Popeza adaswa zitseko zamkuwa,Natyola mipiringidzo yacitsulo.
17 Anthu opusa azunzika cifukwa ca zolakwa zao,Ndi cifukwa ca mphulupulu zao.
18 Mtima wao unyansidwa naco cakudya ciri conse;Ndipo ayandikira zipata za imfa.
19 Pamenepo apfuulira kwa Yehova m'kusauka kwao,Ndipo awapulumutsa m'kupsinjika kwao.
20 Atumiza mau ace nawaciritsa,Nawapulumutsa ku cionongeko cao.
21 Ayamike Yehova cifukwa ca cifundo cace,Ndi zodabwiza zace za kwa ana a anthu!
22 Ndipo apereke nsembe zaciyamiko,Nafotokozere nchito zace ndi kupfuula mokondwera.