23 Iwo akutsikira kunyanja nalowa m'zombo,Akucita nchito zao pa madzi akuru;
24 Iwowa apenya nchito za Yehova,Ndi zodabwiza zace m'madzi ozama.
25 Popeza anena, nautsa namondwe,Amene autsa mafunde ace.
26 Akwera kuthambo, atsikira kozama;Mtima wao usungunuka naco coipaco.
27 Adzandira napambanitsa miyendo ngati munthu woledzeta,Nathedwa nzeru konse.
28 Pamenepo apfuulira kwa Yehova m'kusauka kwao,Ndipo awaturutsa m'kupsinjika kwao.
29 Asanduliza namondwe akhale bata,Kotero kuti mafunde ace atonthole.