26 Akwera kuthambo, atsikira kozama;Mtima wao usungunuka naco coipaco.
27 Adzandira napambanitsa miyendo ngati munthu woledzeta,Nathedwa nzeru konse.
28 Pamenepo apfuulira kwa Yehova m'kusauka kwao,Ndipo awaturutsa m'kupsinjika kwao.
29 Asanduliza namondwe akhale bata,Kotero kuti mafunde ace atonthole.
30 Pamenepo akondwera, popeza pagwabata;Ndipo Iye awatsogolera kudooko afumko.
31 Ayamike Yehova cifukwa ca cifundo cace,Ndi zodabwiza zace za kwa ana a anthu!
32 Amkwezenso mu msonkhano wa anthu,Namlemekeze pokhala akulu.