3 Nawasokolotsa kumaiko,Kucokera kum'mawa ndi kumadzulo,Kumpoto ndi kunyanja.
4 Anasokera m'cipululu, m'njira yopanda anthu;Osapeza mudzi wokhalamo.
5 Anamva njala ndi ludzu,Moyo wao unakomoka m'kati mwao.
6 Pamenepo anapfuulira kwa Yehova mumsauko mwao,Ndipo anawalanditsa m'kupsinjika kwao.
7 Ndipo anawatsogolera pa njira yolunjika,Kuti amuke ku mudzi wokhalamo.
8 Ayamike Yehova cifukwa ca cifundo cace,Ndi zodabwiza zace za kwa ana a anthu!
9 Pakuti akhutitsa mtima wolakalaka,Nadzaza mtima wanjala ndi zabwino.