33 Asanduliza mitsinje ikhale cipululu,Ndi akasupe a madzi akhale nthaka youma;
34 Dziko lazipatso, likhale lakhulo,Cifukwa ca coipa ca iwo okhalamo.
35 Asanduliza cipululu cikhale tha wale,Ndi dziko louma likhale akasupe a madzi.
36 Ndi apo akhalitsa anjala,Kuti amangeko mudzi wokhalamo anthu;
37 Nafese m'minda, naoke mipesa,Ndiyo vakubata zipatso zolemeza.
38 Ndipo awadalitsa, kotero kuti, acuruka kwambiri;Osacepsanso zoweta zao.
39 Koma acepanso, nawerama,Cifukwa ca cisautso, coipa ndi cisoni.