40 Atsanulira cimpepulo pa akulu,Nawasokeretsa m'cipululu mopanda njira.
41 Koma aika waumphawi pamsanje posazunzika,Nampatsa mabanja ngati gulu la nkhosa.
42 Oongoka mtima adzaciona nadzasekera;Koma cosalungama conse citseka pakamwa pace.
43 Wokhala nazo nzeru asamalire izi,Ndipo azindikire zacifundo za Yehova,