5 Anamva njala ndi ludzu,Moyo wao unakomoka m'kati mwao.
6 Pamenepo anapfuulira kwa Yehova mumsauko mwao,Ndipo anawalanditsa m'kupsinjika kwao.
7 Ndipo anawatsogolera pa njira yolunjika,Kuti amuke ku mudzi wokhalamo.
8 Ayamike Yehova cifukwa ca cifundo cace,Ndi zodabwiza zace za kwa ana a anthu!
9 Pakuti akhutitsa mtima wolakalaka,Nadzaza mtima wanjala ndi zabwino.
10 Iwo akukhala mumdima ndi mu mthunzi wa imfa,Omangika ndi kuzunzika ndi citsulo;
11 Popeza anapikisana nao mau a Mulungu,Napeputsa uphungu wa Wam'mwambamwamba;