8 Ayamike Yehova cifukwa ca cifundo cace,Ndi zodabwiza zace za kwa ana a anthu!
9 Pakuti akhutitsa mtima wolakalaka,Nadzaza mtima wanjala ndi zabwino.
10 Iwo akukhala mumdima ndi mu mthunzi wa imfa,Omangika ndi kuzunzika ndi citsulo;
11 Popeza anapikisana nao mau a Mulungu,Napeputsa uphungu wa Wam'mwambamwamba;
12 Kotero kuti anagonjetsa mtima wao ndi cobvuta;Iwowa anakhumudwa koma panalibe mthandizi.
13 Pamenepo anapfuulira kwa Yehova mumsauko mwao,Ndipo anawapulumutsa m'kupsinjika kwao.
14 Anawaturutsa mumdima ndi mu mthunzi wa imfa,Nadula zomangira zao.