1 Wakhazikika mtima wanga, Mulungu;Ndidzayimba, inde ndidzayimba zolemekeza, ndiko ulemerero wanga.
2 Galamukani, cisakasa ndi zeze;Ndidzauka ndekha mamawa.
3 Ndidzakuyamikani mwa mitundu ya anthu, Yehova:Ndipo ndidzayimba zakukulemekezani mwa anthu.
4 Pakuti cifundo canu ncacikuru kupitirira kumwamba,Ndi coonadi canu kufikira mitambo.