4 Pakuti cifundo canu ncacikuru kupitirira kumwamba,Ndi coonadi canu kufikira mitambo.
5 Kwezekani pamwamba pa thambo, Mulungu;Ndi ulemerero wanu pamwamba pa dziko lonse lapansi.
6 Kuti okondedwa anu alanditsidwe,Pulumutsani ndi dzanja lanu lamanja ndipo mutibvomereze.
7 Mulungu analankhula m'ciyero cace; ndidzakondwerera:Ndidzagawa Sekemu; ndidzayesa muyeso cigwa ca Sukoti.
8 Gileadi ndi wanga: Manase ndi wanga;Ndi Efraimu ndiye mphamvu ya mutu wanga;Yuda ndiye wolamulira wanga.
9 Moabu ndiye mkhate wanga;Pa Edomu ndidzaponya nsapato yanga;Ndidzapfuulira Filistiya,
10 Adzandifikitsa ndani m'mudzi wa m'linga?Adzanditsogolera ndani ku Edomu?