8 Gileadi ndi wanga: Manase ndi wanga;Ndi Efraimu ndiye mphamvu ya mutu wanga;Yuda ndiye wolamulira wanga.
9 Moabu ndiye mkhate wanga;Pa Edomu ndidzaponya nsapato yanga;Ndidzapfuulira Filistiya,
10 Adzandifikitsa ndani m'mudzi wa m'linga?Adzanditsogolera ndani ku Edomu?
11 Si ndinu Mulungu, amene mwatitayaOsaturuka nao magulu athu?
12 Tithandizeni mumsauko;Pakuti cipulumutso ca munthu ndi cabe.
13 Mwa Mulungu tidzacita molimbika mtima:Ndipo Iye adzapondereza otisautsa.