1 Ndakhulupirira Yehova:Mutani nkunena kwa moyo wanga,Thawirani ku phiri lanu ngati mbalame?
2 Pakuti, onani, oipa akoka uta,Apiringidza mubvi wao pansinga,Kuwaponyera mumdima oongoka mtima.
3 Akapasuka maziko,Wolungama angacitenji?
4 Yehova ali m'Kacisi wace woyera,Yehova, mpando wacifumu wace uli m'Mwamba;Apenyerera ndi maso ace, ayesa ana a anthu ndi zikope zace.