1 Yehova ananena kwa Ambuye wanga, Khalani pa dzanja lamanja langa,Kufikira nditaika adani anu copondapo mapazi anu.
2 Yehova adzatumiza ndodo ya mphamvu yanu kucokera ku Ziyoni;Citani ufumu pakati pa adani anu.
3 Anthu anu adzadzipereka eni ace tsiku la camuna canu:M'moyera mokometsetsa, mobadwira tnatanda kuca,Muli nae mame a ubwana wanu.
4 Yehova walamulira, ndipo sadzasintha,Inu ndinu wansembe kosathaMonga mwa cilongosoko ca Melikizedeke.