1 Haleluya.Ndidzayamika Yehova ndi mtima wonse,Mu upo wa oongoka mtima, ndi mumsonkhano.
2 Nchito za Yehova nzazikuru,Zofunika ndi onse akukondwera nazo.
3 Cocita Iye nca ulemu, ndi ukuru:Ndi cilungamo cace cikhalitsa kosatha.
4 Anacita cokumbukitsa zodabwiza zace;Yehova ndiye wa cisomo ndi nsoni zokoma.