1 Haleluya.Wodala munthu wakuopa Yehova,Wakukondwera kwambiri ndi malamulo ace,
2 Mbeu yace idzakhala yamphamvu pa dziko lapansi;Mbadwo wa oongoka mtima udzadalitsidwa.
3 M'nyumba mwace mudzakhala akatundu ndi cuma:Ndi cilungamo cace cikhala cikhalire.
4 Kuupika kuturukira oongoka mtima mumdima;Iye ndiye wacisomo; ndi wansoni ndi wolungama.
5 Wodala munthu wakudtira cifundo, nakongoletsa;Adzalimbika nao mlandu wace poweruzidwa.