3 M'nyumba mwace mudzakhala akatundu ndi cuma:Ndi cilungamo cace cikhala cikhalire.
4 Kuupika kuturukira oongoka mtima mumdima;Iye ndiye wacisomo; ndi wansoni ndi wolungama.
5 Wodala munthu wakudtira cifundo, nakongoletsa;Adzalimbika nao mlandu wace poweruzidwa.
6 Popeza sadzagwedezeka nthawi zonse:Wolunguna adzakumbukika ku nthawi yosatha.
7 Sadzaopa mbiri yoipa;Mtima wace ngwokhazikika, wakhulupirira Yehova.
8 Mtima wace ngwocirikizika, sadzacita mantha,Kufikira ataona cofuna iye pa iwo omsautsa.
9 Anagawagawa, anapatsa aumphawi;Cilungamo cace cikhalitsa kosatha;Nyanga yace idzakwezeka ndi ulemu.