5 Akunga Yehova Mulungu wathu ndani?Amene akhala pamwamba patali,
6 Nadzicepetsa apenyeZam'mwamba ndi za pa dziko lapansi.
7 Amene autsa wosauka lrumcotsa kupfumbi,Nakweza waumphawi kumcotsa kudzala.
8 Kuti amkhalitse pamodzi ndi akulu,Pamodzi ndi akulu a anthu ace.
9 Asungitsa nyumba mkazi wosaonamwana,Akhale mai wokondwera ndi ana.Haleluya.