1 M'mene Israyeli anaturuka ku Aigupto,Nyumba ya Yakobo kwa anthu a cinenedwe cacilendo;
2 Yuda anakhala malo ace oyera, Israyeli ufumu wace.
3 Nyanjayo inaona, nithawa;Yordano anabwerera m'mbuyo.
4 Mapiri anatumphatumpha ngati nkhosa zamphongo,Timapiri ngati ana a nkhosa.
5 Unathawanji nawe, nyanja iwe?Unabwerereranji m'mbuyo, Yordano iwe?