3 Nyanjayo inaona, nithawa;Yordano anabwerera m'mbuyo.
4 Mapiri anatumphatumpha ngati nkhosa zamphongo,Timapiri ngati ana a nkhosa.
5 Unathawanji nawe, nyanja iwe?Unabwerereranji m'mbuyo, Yordano iwe?
6 Munatumpha-tumphiranji ngati nkhosa zamphongo, mapiri inu?Ngati ana a nkhosa, zitunda inu?
7 Unjenjemere, dziko lapansi iwe, pamaso pa Ambuye,Pamaso pa Mulungu wa Yakobo;
8 Amene anasanduliza thanthwe likhale thawale lamadzi,Nsangalabwi ikhale kasupe wamadzi.