13 Adzadalitsa iwo akuopa Yehova,Ang'ono ndi akuru.
14 Yehova akuonjezereni dalitso, Inu ndi ana anu.
15 Odalitsika inu a kwa Yehova,Wakulenga kumwamba ndi dziko lapansi.
16 Kunena za kumwamba, kumwamba ndiko kwa Yehova;Koma dziko lapansi analipereka kwa ana a anthu.
17 Akufa salemekeza Yehova,Kapena ali yense wakutsikira kuli cete:
18 Koma ife tidzalemekeza YehovaKuyambira tsopano kufikira nthawi yonse.Haleluya.