3 Koma Mulungu wathu ndiye ali m'mwamba;Acita ciri conse cimkonda.
4 Mafano ao ndiwo a siliva ndi golidi,Nchito za manja a anthu.
5 Pakamwa ali napo, koma osalankhula;Maso ali nao, koma osapenya;
6 Makutu ali nao, koma osamva;Mphuno ali nazo, koma osanunkhiza;
7 Manja ali nao, koma osagwira;Mapazi ali nao, koma osayenda;Kapena sanena pammero pao,
8 Adzafanana nao iwo akuwapanga;Ndi onse akuwakhulupirira,
9 Israyeli, khulupirira Yehova:Ndiye mthandizi wao ndi cikopa cao.